'Fredokiss tamumanga chifukwa anasokoneza ndalama zamalonda,' watero mneneri wapolisi

Katswiri oyimba chamba cha 'Hip-hop' Penjani Kalua yemwe amadziwikanso ndi dzina la Fredokiss ali mchitokosi chapolisi mumzinda wa Blantyre.

Fredokiss wamangidwa lachisanu usiku.

Malingana ndi mneneri wapolisi mdziko muno Peter Kalaya, Fredokiss wamangidwa chifukwa akumuganizira kuti sanayendetse bwino ndalama ya bizinezi imene amachita.

Malingana ndi Kalaya, apolisi anatsinidwa khutu ndi anthu ena kuti Fredokiss pamodzi ndi anzake ena anasokoneza ndalama zochitira malonda.

Fredokiss akuganiziridwa kuti anasokoneza ndalama yochitira malonda

Komabe a Kalaya sananene tsatanetsatane wankhaniyi ponena kuti zingasokoneze ntchito yawo yofufuza pankhaniyi.

"Apolisi atafufuza padandaulo limene analandira anapeza kuti Fredokiss pamodzi ndi anzake ena anasokonezadi ndalama. Sindinganene zambiri chifukwa apolisi akadafufuza zankhaniyi," anatero Kalaya.

Kalaya anatinso pakadali pano sanakwanitse kumanga anthu ena, koma ali ndi chikhulupiliro kuti awamanga.

Fredokiss pakadali pano ali mchitokosi chapolisi mumzinda wa Blantyre, ndipo malingana ndi a Kalaya, akaonekera kubwalo lamilandu zofufuza zonse zikatha.

Fredokiss amayenera kutsogolera gulu la achinyamata pa 22 September pa ulendo opita ku Sanjika kukasiya chikalata pamadando awo kuti mtsogoleri wadziko lino Lazarus Chakwera alamule bwalo lamilandu kuti likhululukile John Mussa yemwe ali ku ndende atapezeka olakwa pamulandu opezeka ndi chamba.

Malingana ndi Fredokiss, bwalo lamilandu lidaonetsa kukondera kwake popeleka chigamulo chawo