National

Zonse zili mchimake kuti zipata zapamseu ziyambe kugwila ntchito

Pali chembekezo kuti chipata chapa Mseu (Toll Plaza) chomwe boma linamanga pa Chingeni boma la Ntcheu chikhala chikutsekulidwa Mwezi uno.


Izi zikudza pomwe chipatachi chimayenera kutsekulidwa pa 1 Okotobala koma zinalephera kamba kakusavana pokhudza mitengo yodutsira pa chipatachi.

Chipata cha pa Chingeni


Anthu ena amati mitengo yomwe inayikidwa inali yofuna kulanga Chabe oyendetsa Galimoto, osati yofuna kuthandizana ndi boma.


Pakadali pano, bungwe lowona za miseu la Roads Authority kudzera mwa mneneli wawo lati zokambirana zili mkati ndimbali zonse zokhudziwa khangakhale zonse zili tayale kuti malowa ayambe kugwira ntchito.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button
error: Sorry, you are not allowed to copy this content!!!!